Chichewa Christian Hymns
Hymn 265 MUDZAZE Yesu mtima wanga ndi chikondicho,
MUDZAZE Yesu mtima wanga ndi chikondicho,
Ukhazikike pa Mulungu wosachokapo.
Mwa ine myatse moto wanu wakuyera mbuu,
Utenthemo zoipa zonse zidakhalamo.
Mubweretu nomwe ’Nu munatsika kalelo;
Ndilira Inu mundidzaze mphamvu yanuyo.
Ndikhazikike inetu, mumtima muli mwai,
Ndi Yesu ndikondanetu, si kanthu kena ai.