Chichewa Christian Hymns
Hymn 240 YESU ndiye Mbuye wanga,
YESU ndiye Mbuye wanga,
Ndamva mawu akewo;
Anandilandira ine,
Nandipulumutsatu.
Mwalembedwa mukalata,
Mawu ake omwewo;
Kuti iwo akumvera,
Akalandiridwatu.
Ndinakhala woipadi,
Ndinam’kana kalelo;
Koma Yesu waiwala,
Mphulupulu zangazo.
Wapumitsa mtima wanga,
Kaamba ndaphunziratu;
Mawu ake olembedwa,
Mukalata mwakemo.
Mumvetu abwenzi athu,
Musakanilire’yi;
Yesu ayitana inu,
Zalembedwa zomwezi.