Chichewa Christian Hymns
Hymn 226 BWENZI ndinamkomanayo
BWENZI ndinamkomanayo
Anandikonda kale;
Kukonda kwandigwirako,
M’kukondamo nditsale.
Kumtima kundimangako
Kosamasuka konse;
Ambuye ndine wanutu
Kunthaŵi nthaŵi zonse.
Bwenzi ndinakomanayo
Anandifera yekha,
Anandipatsa moyowo,
Ndatenga ine ndekha.
Zimene ndili nazozi
Nza Yesu mwini zonse,
Ndi moyo wanga wonse ndi
Wakenso nthaŵi zonse.
Bwenzi ndinamkomanayo,
Ndapeza mphamvu zanga,
Zakundisunga inemo,
Ndiyende m’njira mwanga.
Zolemera zoti mbee!
Zindilimbitsa monse;
Ndalema kuno, komweko
N’kupuma nthaŵi zonse.
Bwenzi ndinamkomanayo
Wokoma mtima wake,
Wotsogolera nzeruzo
Zisunga m’njira mwake.
Palibe wondichotsa ‘ne
Kwa Iye wondikonda;
Pamoyo, imfa, nayeyo
Ndilipo nthaŵi zonse.