Chichewa Christian Hymns
Hymn 225 NDIDZAIMBA za Mulungu,
NDIDZAIMBA za Mulungu,
Zakukonda kwakeko;
Anatuma Mwana wake,
Kundifera kalero.
Inde ndidzayimba nyimbo,
Za kukonda kwakeko;
Ndidzayimba ndi angelo,
Akukhala M’mwambamo.
Ndinachita mphulupulu,
Wayiwala zonsezo!
Ndinakhala ndi zoipa,
Wazichotsa zonsezo!
Wandipatsa moyo wake,
Moyo wakuyera mbuu!
Ine ndili mwana wake,
Wandilera inetu.
Ndiyamika Mbuye wanga,
Ndidzam’lemekezabe;
Ndipititsa mbiri yake,
Yakukonda kwakeko.