Chichewa Christian Hymns
Hymn 224 LINDIKOMERA dzina la Ambuye Yesu wanga,
LINDIKOMERA dzina la Ambuye Yesu wanga,
Lisangalatsa, lichiritsa, lin’chotsera mantha.
Dzinalo la Yesu,
Dzinalo la Yesu
Lindikomera dzina la
Mbuye Yesuwanga.
Lichiza mzimu wophwetekwa ukakhale bata,
Lidyetsa mtima wonse, lipumitsa thupi langa.
Nlokoma dzinalo la Yesu, ndilo thanthwe langa,
Chikopa changa, linga langa m’mene ndibisala.
Ambuye ndinu Mbusa, Bwenzi, ndi
Wansembe wanga,
Ndi Mfumu, Moyo, Njira yomwe,
Inde ndimatama,
Tsopano ndibukitsabe chikondi chanu chija,
Pakufa ine Dzina lanu lindilimbikitsa.