Chichewa Christian Hymns
Hymn 196 NDI inetu sinditha’yi
NDI inetu sinditha’yi
Kunenako milanduyi
Kupempha zachisonizi;
Ndagonjatu Mbuyanga’Nu.
(Aa! Mulungu wanga,
Mundilembe pamphumipo:
Chidzakhala chizindikiro
Cha mpumulo ulinkudza ndi Yesu.)
Ndi ine sizitheka’yi
Kuchoka zakuipazi;
Ndisambe m’mwazi wanuwo;
Ndagonjatu Mbuyanga’Nu.
Ndi ine pondibvutapo
Kugwira nazo m’mtimamo,
Mundithandize monsemo;
Ndagonjatu Mbuyanga’Nu.
Ndi ine ndasaukadi,
Zabwino m’mtima zonsezi
Mwa Inu ndingapezezi;
Ndagonjatu Mbuyanga’Nu.
Ndi ine simufuna’yi
Ndingatayike m’mdima bii,
Ndimvere mwandiuzazi
Ndagonjatu Mbuyanga’Nu
Ndi ine, m’mtima Mwanu mbee!
Mokoma ndingakhalebe,
Ndikhale wanu wanudi;
Ndagonjatu Mbuyanga’Nu.
Ndi inetu ndidziŵedi
Chikondi chodabwitsachi
Pansipa ndi Kumwambako;
Ndagonjatu Mbuyanga’Nu