Chichewa Christian Hymns
Hymn 151 UKAPENYA kwa Yesu uliko moyoko,
UKAPENYA kwa Yesu uliko moyoko,
Inde, moyo tsopanopanotu;
Wolakwira upenye kwa Yesu Mbuyeyo,
Kuwombola naferatu ‘we.
Ona! Ona! Onatu!
Kuli moyo kwa yense
Apenya Yesuyo,
Wakuferatu pamtandapo.
Anasenzapo bwanji uchimo wonsewo,
Ngati wanu pa Yesu sulipo?
Bwanji mwazi wakhetsa kutsuka ifetu,
Ngati uwu sutikwanako?
Zilepheradi zonse kugula moyowo,
Koma mwazi wa Yesu Mbuyeyo;
Khulupi’ra mwamphamvu ya
Mlungu wathuyi,
Kuyeretsa’we m’mtima’komo.
Anatheradi pa mtanda ntchito zonsezi,
Zowombola mizimu yathuyi;
Ndipo yense akadza
Mokondwakondwadi,
Moyo apeza kwa Yesuko.