Chichewa Christian Hymns
Hymn 201 NDILINKUDZA kwa Ambuye,
NDILINKUDZA kwa Ambuye,
Ndisauka, ndinachimwa;
Zanga zonse ndizisiya,
Kudzapeza moyo wina.
Yesu ndikhulupirira,
Munafera ine ndemwe;
Mwaumphawi ndipemphera,
Mundipulumutse tere.
Kale ndinalira Inu,
Kale lomwe ndangochimwa;
Mundiitana: “Idza kuno,
Kuti n’kuchotsere tchimo.”
Yesu, n’kupatsani zonse,
Zili zanu zokhazokha;
Thupi lonse mtima womwe,
Mwini wake ndinu nokha.
E, ndikukhulupi’rani,
Ndauwona mwazi wanu;
Tere ndikugwadirani,
Tere ndapachikwa nanu.
Wadza Yesu, wandidzoza,
Ndakonzeka mwa Iyeyu;
Ndine wake, takondana,
Ndiyamika Mbuye Yesu.