Chichewa Christian Hymns
Hymn 490 YESU adza kuwerenga,
YESU adza kuwerenga,
Ana ake abwino,
Ndikuvala zachifumu,
Zakuwalazo zake.
Ana ake angonga,
Nyenyezi za M’mwamba;
Adzawala m’Ufumu,
Wa Mbuye Yesu.
Yesu adza kukundika,
Ana ake a nkhosa;
Ndiye Mbusa wakufatsa,
Nmalezatu Iye.
Kudzachera tsiku lijalo,
Msangatu msanga;
Kudzawala m’mawa wake,
Pompano ponse.