Chichewa Christian Hymns
Hymn 444 YEMWE afesa nalira,
YEMWE afesa nalira,
M’chikonditu mbewuzo;
Osatopa, osagona,
Yesu amadalitsa.
Ona mmera wakukondwa,
Dzinthu zonse dzachanso;
Ona m’minda mwayeratu,
Kukunkha kwayandika.
Fesa mbewu usatope,
Usaope konsetu;
Nkana utapeza vuto,
Udzatuta mokondwa.
Mvula idzathilirapo,
Dzuwa lidzawalira;
Ndi zipatso zidzabala,
Mphamvu ya Mulunguyo.