Chichewa Christian Hymns
Hymn 388 MOMMUNO, Mbuye tionanetu,
MOMMUNO, Mbuye tionanetu,
Mommuno ndizikhudza zanu phee,
Mommuno zachinsinsi zanu mbuu,
Mwa Inu mtima ndipumirabe.
Mommuno, Mbuye, mkate wanuwu,
Mommuno vinyo wakumwambako,
Mommuno zolemera zanga du,
Chisomo chanu ndidzalaŵanso.
Ndilibe wondithangata ‘ne ’yi,
Ndilibe wina wondisunga ’ne;
Zikwaniratu mphamvu zanuzi,
Ine, Ambuye, mphamvu nzanudi.
Tsopano nthaŵi yake phwandoli,
Loyala ili m’gome mwanumu;
Ndidye ndimwere zakukomazi,
Ndiyanjanabe nanu, Mbuyathu.
Chakudya ichi chidzapita du,
Chizindikitsa za Kumwambazo;
Zosapitazo tidzalaŵatu,
Za Yesu mwini wakukondako.
Tikadya phwando zaka zonsezi,
Ndipo zakudya zimalozatu
Kuphwando lija la Kumwambako,
Komwe tidzadya kwa Mulungutu.