Chichewa Christian Hymns
Hymn 381 MONGA zomera zonsezo
MONGA zomera zonsezo
Zikula ponsepo,
Mulungu mumeretsazo,
Momwemo anawo.
Munali mwana, Yesu ’Nu
Wamng’ono kalelo,
Ndi munakula m’msinkhu ndi
Kutama ’Tatewo.
Ndi ife tinga, mbewuzo
Zomera m’mundawo;
Mumtima mutidyetsedi,
Tikule bwinomo;
Ndi kutsukidwa m’mwazimo
Mumtima mwathu mbee,
Tionetsedwe konseko
A Mlungu ana ’ke.