Chichewa Christian Hymns
Hymn 130 PHWANDO la Belisazara,
PHWANDO la Belisazara,
Ndi nduna zake zikwi;
Anamwera zikho za,
Yehova Woopsayo,
Ananyozadi ndithu,
Ukulu wa Yehova;
Ndipo anaonatu,
Dzanja lolemba pakhoma.
Linali dzanja la Mlungu,
Linali dzanja la Mlungu,
Litanthauzanji kodi
Dzanjalo, lolembalo?
Litanthauzanji ‘ko?
Dzanja lolemba pakhoma.
Mfumuyo niitanatu,
Anzeru ake onse;
Kuti ayiuzetu,
Cholinga cha lembalo.
Pofika Danieli,
Nayiuzatu mfumu:
“Ufumu wanu watha.”
Litero lemba pakhoma.
Leronso mbale wangawe,
Usazengerezetu;
Ndi zoipa zakozo,
Zimene uzichita.
Ungadzasiidwetu,
Panthawi yomaliza;
Chenjeratu mbalewe,
Ufumu wako ungathe.