Chichewa Christian Hymns
Hymn 133 NSEMBE yake ya Kaini,
NSEMBE yake ya Kaini,
Inalitu yoipa;
Nsembe yake ya Abele,
Inalitu yabwino.
Ee! Kaini,
Ee! Kaini,
Alikutitu Abele;
Mulungu am’funa.
Lonjezo la Hananiya,
Linam’tengera imfa;
Safiranso mkazi wake,
Nafa pamodzi naye.
Hananiya,
Hananiya,
Zilikutitu zopereka;
Ambuye azifuna.
Nsembe yake ya Mulungu,
Ndi Ambuye Yesuyo;
Anatifera pa mtanda,
Kutipulumutsa fe.
Ee! Mulungu,
Ee! Mulungu,
Napereka Mwana wake;
Kutipulumutsa.
Moyo wathu pothokoza,
Tipereke zoonga;
Potipatsa madalitso,
Timutumikiretu.
E! Mulungu,
E! Mulungu,
Tiperekatu zathuzo;
Mwapangano lathu.