Chichewa Christian Hymns
Hymn 262 “KHALA mwa Ine,” Yesu anatero;
“KHALA mwa Ine,” Yesu anatero;
Mawu abwino, koma Mbuye wanga
Sin’ngathe ndekha, mukhalitse ine
Mwa ’Nu ndikhale nawo moyotu.
“Khale mwa Ine,” munachotsa tsoka,
Mletse Satana anganyenge ine:
Mibvi yamoto yake muizime
M’mtimamo, ndikhulupirire ’Nu.
“Khala mwa Ine,” ndinu mwini mphamvu,
Mundithandize ine ndikafoka;
Mzimu Woyera andiululire
Zoona zanu m’mtima mwangamu.
“Khala mwa Ine,” ndinu mwini moyo.
Nthambi zouma zidulidwa m’mtengo:
Ine wopanda Inu ndifokanso,
Zipatso zikasoŵa msadze ’ne.
“Khala mwa Ine,” Mbuye, ndifunitsa;
Mzimu Woyera mlonge m’mtima mwanga,
Akagonjetsetu machimo anga,
Mtima woyera andipatsenso.