Chichewa Christian Hymns
Hymn 419 ANYAMATA a Mulungu,
ANYAMATA a Mulungu,
Muzigwira nkhondoyo,
Mumenyane ndi Satana
Mzimu wakunyengayo.
Komwe asauka anthu
Akukhala m’mdimamo
Osadziŵa Mpulumutsi,
Phunzitsani konseko.
Pomangidwa anthu nayo
M’yambo yoipitsayo,
Pomwe amaopa chabe,
Masulani golilo.
Walitsani nyali yanu
Ikachotse mdima bii!
Mpaka ikainga zonse
Zosautsa m’dzikoli
Akutopa ndi ofoka
M’ŵatonthoze mtima phee!
Osokera, onyozeka
Muŵafunefunebe.
Achisoni obvutidwa,
M’ŵathandize msangatu;
Zosautsa zawo zonse
Yesu azichotsadi.
Anyamata limbikani,
Gwiranitu nkhondoyi;
Yes salephera mwini,
Sitiiŵalira ’yi.
Isaleke ntchito yake
Mpaka anthu onsewo
Alambira Mfumu yathu,
Nagonjera konseko.