Chichewa Christian Hymns
Hymn 366 MADZULO aja kalero
MADZULO aja kalero
Odwala anagona duu;
Opwetekedwa nthendazo
Munachiritsa Inutu.
Tsopano lino kwada bii,
Nafenso timva m’mtimamo;
Simuoneka, komatu
Tidziŵa muli nafedi.
Wopulumutsa mudzetu;
Adwala ena m’mtima bii,
Ena sakukondani ’Nu,
Ena sasamalira ’yi.
Ndi ena sanamvera ’yi
Enanso alemedwatu,
Zoopsya nazo tifadi;
Mukadza tidzaposatu.
Wopulumutsa, Inunso
Munasauka kalelo;
Muona zoda m’mtimamo
Tibisa ndi manyaziwo.
Mutichiritse ifenso,
Mutiphunzitse zanuzi;
Timve tsopano mawuwo
Ochiza nthenda yathuyi.