Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 88 Yesu, dzina lakukonda,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 88 Yesu, dzina lakukonda,

 

Yesu, dzina lakukonda,
Lopambana onse ena,
Tonse tidzaligwadira
Ndi mitima yochepetsa.

Yesu, dzina lokondwetsa
Akuipa a padziko,
Kale linatidziŵitsa
Mpulumutsi ndiye Yesu.

Yesu dzina lakufatsa,
Anamutcha ’kali Mwana,
M’mene analoŵa kale
M’dziko lino lakudana.

Yesu, dzina ndi lomweli
La pa dziko lino lonse,
Ndi lamphamvu yolanditsa
Anthu mu masoka onse.

Yesu, dzina lakukonda
La Mwanayo wa Mulungu,
Ife anthu osauka
Tithaŵira nalo kwanu.

Exit mobile version