Chichewa Christian Hymns
Hymn 81 MBUYE Yesu adzabwera,
MBUYE Yesu adzabwera,
Asekere anthu onse;
Mawu awa achimwemwe
Azimveka m’dziko lonse.
Adzabwera, adzabwera;
E! bwerani Mbuye wathu.
Dziko lino linaona
Masauko a Mbuyathu,
Lidzaonanso ulemu,
M’mene adzabwera Iye.
Adzabwera, adzabwera;
Timvomera, E! mubwere
Anthu anu amafoka,
Pa ulendo nasokera;
Ha! Adzaonana nanu
Atabvalanso zoyera.
Mudzabwera, mudzabwera;
Inde Mbuyetu mubwere.
Ndi chiyembekezo ichi
Sitikhala chete ife:
Tiimbitsa nyimbo zathu
Zakulemekeza Mlungu.
Adzabwera, adzabwera
E!! mubwere msanga YESU.
