Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 77 MMENE Yesu adzabwera,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 77 MMENE Yesu adzabwera,

 

MMENE Yesu adzabwera,
Adza ndi mitambo;
Ndipo diso lililonse,
Lidzamuwona Iye.

Adza, adza,
Adza ndi mitambo,
Ndipo diso lililonse;
Lidzamuwona Iye.

Adzakhala pa chimpando,
Choweruziracho;
Nadzayamba kuweruza,
Milandu ya anthu’fe.

Angelo ‘dzagwira ntchito,
Yolekanitsadi;
Anthu onse a padziko,
M’magulu awiritu.

Olugama nadzayima,
Kudzanja lamanja;
Koma onse oyipawo,
Mbali yakumanzere.

Akudzanja lamanjalo,
Kumoyo wosatha;
Akudzanja lamanzere,
Kumoto Wosathawo.

Exit mobile version