Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 71 DZIKO lino lapansi, ndilibetu abwenzi,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 71 DZIKO lino lapansi, ndilibetu abwenzi,

 

DZIKO lino lapansi, ndilibetu abwenzi,
Ndili ndekha mpanjira n’kwaŵenitu;
Ndilibetu chakudya, ndilibetu chakumwa,
Ndingoyenda mpanjira n’kwaŵenitu.

N’kwawenitu,
N’kwawenitu,
Dziko lino sikwathu
N’kwaŵenitu.

Dziko lino lapansi mavuto ndi osatha,
Ine sindingalithe n’kwaŵenitu;
Ukasowa chumacho, abwenzi akuthawa,
Koma kwathu satero n’kwaŵenitu.

Anyamata, ‘sungwana
Samaopa Mulungu,
Sichifukwa chinanso n’kwaŵenitu;
Abambo ndi amayi
Samaopa Mulungu,
Sichifukwa chinanso n’kwaŵenitu.

Tiyeni abale ‘fe tiyang’ane kwa Yesu,
Yemwe angatipatse moyowotu;
Moyo uno wam’dziko abale ndi wozunza,
Moyo wokoma ndiwo wa Yesuyo.

Exit mobile version