Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 70 LAMBIRA, Mfumuyo,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 70 LAMBIRA, Mfumuyo,

 

LAMBIRA, Mfumuyo,
Ndi Yesu Mbuyathu,
Tamvani nyimbo za ‘mithenga aKumwambako;
Nafenso pansipa
Tim’yamikire ’Ye,
Ndi Mpulumutsi wathu wotifera kalero.

Lambira Yesuyo,
Wokonda tonsefe;
Mabala ake achikondi awonekabe;
Tisayiwale ’yi
Zoŵaŵa zakezo,
Tileke kum’chimwira, kum’sautsa Yesuyo.

Lambira Yesuyo,
Uthenga wakewu
Uyanjanitsa anthu onse m’dziko munomo:
Amaiŵala za
Kudana kwawoko,
Nayamikira Mfumu yamtendere monsemo.

Lambira Mfumuyo
Wolenga zonsezi:
Nyenyezi, dziko, dzuŵa, mwezi ndi mitamboyi;
Tikweze dzinalo
La Mbuye Yesuyo,
Tim’yamikire pansi pano ndi Kumwambako.

Exit mobile version