Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 7 NDI Aleluya imbirani,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 7 NDI Aleluya imbirani,

 

NDI Aleluya imbirani,
“Tate wathu wa Kumwamba,
Analenga zonse;
Chifundo chake chachikulu,
Nzeru, mphamvu ndi ufumu,
Tiyamike tonse.

Ndi Aleluya imbirani,
Yesu Khrisitu Mpulumutsi,
Anachoka kwawo;
Nakhala munthu pansi pano,
Nasawuka, natifera,
Natisiira mawu.

Ndi Aleluya imbirani,
Mzimu wake wakuyera,
Amakhala nafe:
Atilangiza za Mulungu,
Nayeretsanso mitima,
Ya Akhrisitu ife.

Mulungu wathu tiyamika,
“Tate, Mwana,
Mzimu yemwe,
Aleluya Inu;
Woyera Inu, ndi wamphamvu,
Muyenera anthu onse,
Agwadire Inu.

Exit mobile version