Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 64 LERO Kristu anauka,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 64 LERO Kristu anauka,

 

LERO Kristu anauka,
Aleluya.
Ndilo tsiku lokondwera.
Aleluya.
Iye kale anafera,
Aleluya.
Nawombola otaika,
Aleluya.

Timwimbire zomtamanda
Aleluya.
Ndiye Kristu wa Kumwamba
Aleluya.
Natsikira kumanda,
Aleluya.
Nalanditsa akuipa.
Aleluya

Koma masauko ake,
Aleluya.
Anatiwombola ife.
Aleluya.
Ndiye Mfumu ya mafumu,
Aleluya.
Mwana ndithu wa Mulungu.
Aleluya.

Timwimbire Mulungu wathu,
Aleluya.
Kuti atikonda ndithu:
Aleluya.
Mtamenso angelo inu,
Aleluya.
Ndiye ‘Tate, Mwana, Mzimu
Aleluya.

Exit mobile version