Chichewa Christian Hymns
Hymn 61 A! MUTU wakuyera,
A! MUTU wakuyera,
Wolaswa wachisoni,
Abveka Inu anthu
Ndi minga ya udani;
Ambuye mwafokatu
Ndi masauko aja,
Mwatuŵa m’maso mwanu
Mumayerera kale.
Ambuye Mwini moyo,
Kokoma mnafumako;
Ndizizwa pomva mawu
Umo mwachitiramo.
Chisoni chija chanu
Ncha pamachimo anga,
Mwasaukira Inu
Kupalamula kwanga.
Nditani! Bwezi langa
Kulemekeza Inu
Chifukwa cha chifundo
Ndi imfa ija yanu?
Mundikhalitse wanu,
Wokhulupira inu;
Musandilole konse
Kufulatira Inu.
Pakufa ine Mbuye
Mukhaletu pafupi,
Mundithandize ine,
E, mudzandimasula;
Ndipenyetsetsa Yesu,
Ambuye Mfumu yanga,
Ndikafa ndine wanu,
Ndikhale nanu m’Mwamba.
