Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 6 LEMEKEZA Mulungu ’Tate,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 6 LEMEKEZA Mulungu ’Tate,

 

LEMEKEZA Mulungu ’Tate,
Lemekeza Mulungu Mwana,
Lemekeza Mulungu Mzimu,
Mulungu Mmodzi ndi wamkulu,
Lemekeza, lemekeza
Mulungu wathu yemweyo.

Mlemekeze, anakonda
Natitsuka m’mtima mwathu;
Anatiwombola ife
Tikakhale ndi chifumu.
Lemekeza, lemekeza
Yesu Mbuye Nsembeyo.

Lemekeza Mfumu yathu,
Mfumu ya mipingo yonse,
Ipambana anthu onse
Akumwamba ndi apansi.
Lemekeza, lemekeza
Mfumu ya mafumuyo

Exit mobile version