Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 57 TIYENI, dzalireni nane,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 57 TIYENI, dzalireni nane,

 

TIYENI, dzalireni nane,
Tidze ku mtanda wa Ambuye,
Tionse tichitetu maliro;
Wapachikidwa Ambuyathu.

Kodi misozi itisoŵa,
Poona anthu amanyoza?
Onani umo apirira;
Wapachikidwa Ambuyathu.

Anena mawu m’mtanda momwe
Mawu ochepa achifundo,
Apempherera ’dani ake;
Wapachikidwa Ambuyathu.

Mtima wangawe, uyenera
Kuduka ndi manyazi lero,
Zamlasa ndi zoipa zako;
Wapachikidwa Ambuyathu.

Ona chikondi cha Mulungu,
Ona zoipazo za anthu,
Koma chakula ndi chikondi;
Wapachikidwa Ambuyathu.

Exit mobile version