Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 51 PANTHAWI yakufa Ambuye,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 51 PANTHAWI yakufa Ambuye,

 

PANTHAWI yakufa Ambuye,
Anthu ananena:
“Dzipulumutsetu pamtandapo.”

(M) Yesu ndi mawu aakulu,
(O) Anafuula;
(M) Yesu ndi mawu aakulu,
(O)Anafuula;
“Eloyi, Eloyi
Mulungu wanga,
Mwandisiiranji,
Mwandisiiranji?”

Imfa ya Bwenzi lathu Yesu,
Yomvetsa chisoni;
Ophunzira onse anathaŵa.

Pamene anakhomedwatu,
Pamtanda Yesuyo;
Zoipa zathu zinam’psinja ‘Ye.

Imfa yake ndi yopambana,
Yotipulumutsa;
Yotitengera ife mtendere.

Exit mobile version