Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 497 TILIKUIMBA nyimbo yomweyi,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 497 TILIKUIMBA nyimbo yomweyi,

 

TILIKUIMBA nyimbo yomweyi,
Yakuyamika Mbuye wathuyo;
Mtendere wake tiufunadi,
Titapemphera tinke kwathuko.

Titanka kwathu mkhale nafeko,
Tikufunani Yesu Mbuyathu;
Musunge ife nthaŵi zonsezo,
Mutiyeretse m’mtima mwathu mbuu!

Usiku uno mutisungedi,
Khalani m’fupi m’nyumba mwathumo;
Mamaŵanso mudzatidzutse nji!
Kuti tigwire ntchito zathuzo.

Mtitsogolere nthaŵi zonsezo;
Kuyenda tokha sitikhoza ’yi,
Ngati mukhala Mbuye m’fupimo,
Sitidzaopa kanthu kena ’yi.

Exit mobile version