Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 495 MLUNGU dalitsani Malaŵi,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 495 MLUNGU dalitsani Malaŵi,

 

MLUNGU dalitsani Malaŵi,
Mumsunge m’mtendere;
Gonjetsani adani onse,
Njala, nthenda, nsanje;
Lunzitsani mitima yathu
Kuti tisaope,
Mdalitse Mtsogoleri, nafe,
Ndi Mayi Malaŵi.

Malaŵi dziko lokongola,
La chonde ndi ufulu,
Nyanja ndi mphepo ya m’mapiri,
Ndithudi tadala;
Zigwa, mapiri, nthaka, dzinthu,
Mphatso zaulere;
Nkhalango, madambo abwino,
Ngwokoma Malaŵi.

O! Ufulu tigwirizane
Kukweza Malaŵi;
Ndi chikondi, khama, kumvera,
Timutumikire;
Pankhondo nkana pa mtendere
Cholinga n’chimodzi,
Mayi, Bambo, tidzipereke
Pokweza Malaŵi.

Exit mobile version