Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 481 USACHIMWE konse,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 481 USACHIMWE konse,

 

USACHIMWE konse,
Lekatu kukwiya;
Uli mwana wake,
Mwana wa Mbuyathu.

Yesu ndi wofatsa,
Yesu ndi woyera;
Ana ake omwe
Aziyera m’mtima

Mzimu wakuipa
Ukusuzumira,
Umakuyesera
Kuti ukachimwe.

Koma usalole
Mawu a Satana;
Bweza tchimo lake,
Chita zolungama.

Yesu ndi Mbuyako,
Mbuyeyo ngwabwino;
Ana ake omwe
Aziyera m’mtima.

Exit mobile version