Chichewa Christian Hymns
Hymn 48 IMFA ya Mwana wa Mulungu,
IMFA ya Mwana wa Mulungu,
Inali yomvetsatu chisoni;
Anatifera pa mtandapo,
Kutiwombola kumachimo.
Chinsalu cha m’kachisi
Chinang’ambika pakati
Ndi pempho la
M’dzina la! Tate,
Ndi Mwana ndi Mzimunso.
Mbuye Yesu ponka
Kumwamba,
Nanena, “ndikupita kwa “Tate;
Kukakukonzerani malo,
Ndipo Ine ndidzabweranso.
“Koma mudzalandira mphamvu,
Mzimu Woyera ‘tadza pa Inu”;
Ndipo tonsefe ndife mboni,
Kutitu Mzimu ndi Nkhosweyo.
