Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 468 NDIKONDWA kuti

Chichewa Christian Hymns

Hymn 468 NDIKONDWA kuti

 

NDIKONDWA kuti
Atate wa M’mwamba,
Atidziwitsa chikondi chakecho;
Ndimaŵerenga m’Uthenga Wabwino,
Kuti Ambuye akonda ana ‘ke.

Ndikondwa kuti Yesu akonda,
Yesu akonda, andikondabe;
Ndikondwa kuti Yesu akonda,
Amandikondabe.

Yesu ndim’konda, akondanso ine,
Anandifera pamtanda woopsa;
Wosayenera, woipa ndi
Tsoka langalo Ambuye nachotsa.

Mzimu Woyera akhala mwa ine,
Atsimikiza chikondi cha Yesu:
Ine n’tachimwa amandikumbutsa,
“Lapa mwana we akukonda Yesu.”

Ndikadzawona Ambuye Kumwamba,
Sindidzawopa pokhala akonda:
Anandikonzera kalelo nyumba,
Ndidzakhalamo wokondwa, wokoma.

Exit mobile version