Chichewa Christian Hymns
Hymn 452 MLUNGU, Inutu,
MLUNGU, Inutu,
Mwalenga dzuŵali,
Nyenyezi, mwezi mbee,
Ndi dzikoli.
Koma ineyu
Simuiŵala ’yi;
Mundisamala ’ne
Ndisagwe ’yi.
Mbuye, Msungi ’Nu,
Mutuma indedi
Za moyo wangawu
Zokomazi.
Yesu Mwanatu
Anafa imfayo
Achotsa zoti bii;
Nadzukanso;
Kuti m’Mwambamo
Ndikatamandetu
Wondisamalabe,
Mbuyangayu.
