Chichewa Christian Hymns
Hymn 450 YESU, munditsogoza
YESU, munditsogoza
M’njira yanga yonseyo;
Wakunditsogozatu
Ndinu, mundisungetu;
Inde, paulendowo
Mundisunge kolimba.
Monga may’asusunza
Mwana wake polira,
Wakunditonthozatu
Ndinu, munditonthoze,
Ine, m’njira yanuyi
Munditsogoleretu.
Mbuye, ndinu wamphamvu,
Mumatola ananu.
Anthu onse pansipa
Ali otaikatu;
Muchitire chifundo,
Muŵatole onsewo.
