Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 447 OYAMIKA Mlungu m’bwere,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 447 OYAMIKA Mlungu m’bwere,

 

OYAMIKA Mlungu m’bwere,
Zamasika mudzayimbe;
Dzinthu dzathu takolola,
Sidzionongeka m’minda.
Mlungu Mlengi asamala,
Zotisowa akonzera;
M’lowe m’nyumba ya Chauta.
M’kweze nyimbo zamasika.

Dziko lonse n’la Mulungu,
Kuti lim’balire dzinthu;
M’munda zonse zimamera,
Zakukoma ndi zoipa.
Mmera udza, bwino ngala,
Maso omwe amakhwima;
Mutilole, mwini dzinthu,
Tikakhale dzinthu dzanu.

Adzabwera Mbuye wathu,
Kukolola dzinthu dzake;
M’munda mwake akachotse,
Minga ndi zoipa zonse.
Adzatumanso angelo,
Minga akaponye m’moto;
Koma tirigu amsunge,
M’nkhokwe yake nthawi zonse.

Exit mobile version