Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 446 YAMIKANI nonse ’nu,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 446 YAMIKANI nonse ’nu,

 

YAMIKANI nonse ’nu,
Pomwimbira nyimbozi
Za masika athuwa;
Potumiza mvulayi,
Mlungu wathu yemwedi
Atipatsa zonsezi;
Timwimbire m’nyumbayi
Za masika athuwa.

Dziko lathu lonseli
Nla Mulungu yemweyu;
Atumiza mphatsozi
Zakutilimbitsadi,
Mmera wathu wonsewu,
Mbewu zathu zonsezi;
Timtamande Mbuyeyu
Wotipatsa zonsezi.

Nthaŵi yina Mbuyeyu
Adzafika pansipa,
Nadzakonza zonsetu;
Zosakondweretsazi
Naziponya m’motowo,
Koma m’nkhokwe mwakemo
Mudzadzala mbewu tho!
Zokomera bwinotu.

’Dzani Mbuye msangatu,
Msonkhanitse zonse phe;
Anthu anu onsewa,
Muwapulumutse ’wo
Zopweteka zawozo,
Ziwathera zonse phe!
’Dzani mu Ufumu ndi,
K’wasonkhanitsa onse.

Exit mobile version