Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 433 MULUNGU wa Kumwamba bwera kunoku

Chichewa Christian Hymns

Hymn 433 MULUNGU wa Kumwamba bwera kunoku

 

MULUNGU wa Kumwamba bwera kunoku
Ndi mtima wokondwera kuloŵa m’nyumbayi;
Chifukwa cha zabwino mwatichitirazi
Tikukuyamikirani leroli.

Inde, tikuyamikani, Atate, leroli,
Mwatimangira ’fe kuno kachisi wanuyu!
Ndi ulemerero wanu mudzaze m’nyumbayi;
Muyeretse, mudalitse munomu.

Tikondwa tonse ndikukuthokozani ’Nu
Poyamba kupemphera ndikuimbira ’mu;
Mommuno nsiku zonse mukhale nafetu,
Monga ndi angelo anu m’Mwambamo.

Ikhale ngati nyali yoŵala nyumbayi,
Yakutsogoza onse ophunthwa m’mdima bii;
Akunja ndi Akristu m’ŵapulumutse ndi
Kuunika kotuluka munomu.

Exit mobile version