Chichewa Christian Hymns
Hymn 431 AKAPANDA kumanga,
AKAPANDA kumanga,
Nyumba Yehovayo;
Woyimanga nyumbayo,
Angomanga chabe.
Gwirani ntchito yake,
Ndi mapemphero;
Kuti Yehova adalitse,
Ntchito yanu.
Ngati mugwira ntchito,
Ndi nzeru zanuzo;
Mulibe phindu ndithu,
Pamaso pa Mbuye.
Tipempha ‘Nu Yehova,
M’dalitsetu ntchito;
Zathu kuti Ufumu,
Wanu Ukwezedwe.
