Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 422 DZIKO lonse lapansi,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 422 DZIKO lonse lapansi,

 

DZIKO lonse lapansi,
Linachimwa kwa Mlungu,
Chilango chake ndicho cha imfa;
Koma podza Yesuyo,
Anathetsa mlanduwo;
Potifera ife pamtandapo.

Onani,
Mwana wa Nkhosa,
Wachotsa tchimo lonse pansipa;
Ndiye Yesu Mfumuyo,
Ndiye Mpulumutsiyo;
Wotifera ife pamtandapo.

Tsono mmene tadziwa,
Kuti ndife ochimwa,
Tiyeni tinke kwa Ambuyewo;
Tisachite manyazi,
Tiwauze tchimolo;
Iwo adzatikhululukira.

Wotikhululukira,
Adzatiwuza tonse,
Kuti tisadzachimwenso ndithu;
Zakale zatha ndithu,
Zatsala zatsopano;
Tasamba mwazi wake tayera.

Exit mobile version