Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 413 ZIPATA zachitsulo zitseguke zonse mbee!

Chichewa Christian Hymns

Hymn 413 ZIPATA zachitsulo zitseguke zonse mbee!

 

ZIPATA zachitsulo zitseguke zonse mbee!
Ambuye wa Kumwambako aloŵe momwemo.

Mbendera yake ikupiza m’mlengalengamo,
Kufana ndi nyenyezi younika m’mdimamo.

Ankondo a Mulungu ’nu,
Yendani m’njiramo,
Mitima yanu yonseyo iyeretsedwe mbuu!

Tsatani Mbuye Yesuyo ndi mtanda wakewo;
Mlaliketu Uthenga kwa anthu onsewo.

Musamaopa kanthu ’yi tamani Yesuyo;
Kaimbireni nyimboyi ndi mphamvu zonse.

Zipata zatsegudwa mbee! za m’dziko monsemo;
Ambuye wapambanatu ndi mtanda wakewo.

Exit mobile version