Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 41 MKATI mwa zovuta zathu

Chichewa Christian Hymns

Hymn 41 MKATI mwa zovuta zathu

 

MKATI mwa zovuta zathu
Yesu aitana ife,
Tsiku lonse amanena:
“Tsata Ine mkristu iwe.”

Kale ophunzira ake
Namvanso kunyanja kwawo,
Zinthu zonse anasiya
Kukatsata Mbuye wawo.

Yesu atiuze ife;
Tikakonda chuma chokha,
Ati Yesu; “Mwana wanga,
Undikondetu koposa.”

Mwachimwemwe, mwachisoni,
Pogwiritsa ntchito zonse,
Aitana Mpulumutsi
Kuti tizimkonda tonse.

Yesu ayitana ife;
Mbuye, mutimvetse ndithu,
Tipereke mtima wathu,
Tikondane lero ndithu.

Exit mobile version