Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 409 ANTHU akum’maŵa

Chichewa Christian Hymns

Hymn 409 ANTHU akum’maŵa

 

ANTHU akum’maŵa
Nanka msangako,
Nzeru ’nali nazo,
Nafatsansowo;
Nanka kuli Mwana
Anabadwayo;
Anatsogozedwa
Ndi nyenyeziyo.

Anapeza Mwana
Ali m’kholamo,
Nagwadira Iwo
Mbuye wawoyo;
Anthu onse omwe
Ali pansipa,
Azitsata Mbuye
Ndi nyenyeziyo.

Mu ulemerero,
Yesu m’Mwambamo
Muli eni ake;
Anthu onsewo
Osadziŵa konse,
Akutalinso,
Akokedwe iwo
Ndi nyenyeziyo.

Akukhala kunja,
Osokeranso,
M’ŵaŵalire Mbuye,
Asagone’wo;
Amumdima omwe,
Olemedwanso,
Mtsogoleri wawo
Ndi nyenyeziyo.

Paulendo wathu
Tili pansipa,
Muŵalire tonse
Tili m’njiramo;
Mutitsogolere
Anthu tonsefe,
Mutifitse tonse
Ndi nyenyeziyo.

Exit mobile version