Chichewa Christian Hymns
Hymn 406 M’MENE umauka m’maŵa,
M’MENE umauka m’maŵa,
Sunagwire ntchitozo,
Sunayambe kukayenda,
Ugwadire Mlunguyo.
Pena uli kusekera,
Pena nkhaŵa m’mtimamo,
Wachimwemwe, wachisoni,
Uza Yesu zonsezo.
Wakuchezacheza naye
Ukagwira ntchitozo;
Pakukumbukira Yesu,
Nkhaŵa zidzachokanso
Ndi zapansi zikafuna
Kukudzaza m’mtimamo,
Utsogole kopemphera,
Uza Yesu zonsezo.
Ndi m’kutero udzadziŵa
Chifuniro chakecho; Iye adzakuthandiza
Uthangate enanso:
Ndi ofoka ulimbitse,
Akulapa bwezatu;
Ndi za ntchito zake izi
Uza Yesu zonsezo.
Ndipo ngati ungolema,
Ulefuka m’dzulomo,
Ndi Satana akayesa
Kukukola m’mtimamo:
Wakufoka, wakuopa,
Penyetsetsa Iyeyo;
Udzakhazikika m’mtima
Pakumuza zonsezo.
