Chichewa Christian Hymns
Hymn 405 POLENGA dzikoli
POLENGA dzikoli
Pakumva Inudi,
Kwayeratu;
Mumve pempheroli,
Ndipo pamenepo
Palibe mawuwo,
Muŵaletu.
Inu wakudzatu
Kuŵachiritsadi
Anthendawo,
Kupatsa moyowo,
Kuona m’masomo,
Pa anthu onsewo
Muŵaletu.
Mzimu woonadi
Ndi wachikondicho,
Idzanitu;
Muunikirepo
Pali zamdimazo,
Pa dziko ponsepo
Muŵaletu.
Inu atatuwo,
Wodala Mlunguyo,
Timveretu;
Pa dziko ponsepo
Muchotse mdimawo,
Mutume Mawuwo,
Muŵaletu.
