Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 4 INU Mulungu, tikuyamikani;

Chichewa Christian Hymns

Hymn 4 INU Mulungu, tikuyamikani;

 

INU Mulungu, tikuyamikani;
Tivomereza ndinu Ambuyathu;
Ponse, atate, akugwadirani,

Nanu akukuzani amithenga,
Nanu zam’mwamba ndi zamphamvu zake,
Nanu angelo a mitundu yonse
Akuimbirani:

“Mbuye Woyera! E, Woyera nokha!
Mbuye Woyera! Mbuye wa makamu!
Ponse ulemu wanu ndi wodzaza;
Pansi ndi Kumwamba.”

Inu atumwi akumweka aja,
Ndi aneneri oyanjana omwe;
Ndi aunyinji anakuferani;
Akuyamikani.

Mpingo Woyera! wa kwa anthu onse;
Ukumverani, Mfumu ndi Atate,
Mwana woona wa ulemu wonse,
Mzimu, Nkhoswe yemwe.

Khristu Mfumuyo yaulemerero!
Mwana wosatha wa Atate ndinu!
Simunanyoza mimba ya Namwali;
Potipulumutsa.

Imfa mutagonjetsa ndi zoŵaŵa.
Njira munatsegula tikaloŵe;
Momwe mukhala Inu ndi Atate;
Mu ulemerero

Kumva milandu yathu mudzabwera;
Mutithandize, atumiki anu;
Mwatiwombola nawo mwazi wanu;
Mutipulumutse.

M’tiŵerengere
M’Mwamba ndi oyera;
Mutidalitse, ndi’fe anthu anu;
Moyo wosatha, mutipatse tonse;
Mutilamulire.

Tsiku ndi Tsiku timalemekeza;
Nanu tikukuzani osaleka;
Mbuye, m’tisunge tingachimwe lero;
M’tichitire nsisi.

Mbuye, chifundo chanu chitigwere;
Monga tikhulupi’ra inu nokha;
Takhulupi’ra zedi mwa’Nu, Mbuye;
Tisagome konse!

Exit mobile version