Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 391 MUNDIMVERE, Mbuye wanga

Chichewa Christian Hymns

Hymn 391 MUNDIMVERE, Mbuye wanga

 

MUNDIMVERE, Mbuye wanga
Nkana ine ndimalakwa,
Koma ndinu moyo wanga;
Mbuye, mkhale ndine.

Ndine mlendo pansi pano,
Msanditaye m’dzanja lanu,
Mundisunge mwana wanu;
Mbuye, mkhale ndine.

Munafera ine kale
Kuti mukandimasule,
Lero lino mndinyamule;
Mbuye, mkhale ndine.

Mundidzaze ndi chikondi,
Mndiyeretse m’mtima monse,
Chifuniro changa mthyole;
Mbuye, mkhale ndine.

Imfa ikandifikira,
Inu ndidzakangamira
Ndikaloŵa ine m’mdima,
Mbuye, mkhale ndine.

Exit mobile version