Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 390 A! YESU, ndapangana

Chichewa Christian Hymns

Hymn 390 A! YESU, ndapangana

 

A! YESU, ndapangana
Kutumikira ’Nu
Ndi moyo wanga wonse,
Mbuyanga ndinutu;
Mukhaletu pafupi
Masiku onsewo,
Sindidzaopa konse,
Mutsogolereko.

Ndikufuna kumva Inu,
E, Mawu anuwo,
Ndisamve za satana
Zonyenga zakezo;
Adani anga onse
Andizingiratu;
Mukhaletu pafupi,
Mundithangate ’Nu.

A! Yesu mwapangana
Ndi anthu anuwo
Adzakhala ndinu
Ku Dziko lanulo;
Inenso ndapangana
Ndisabwerere ’yi;
Mndipatse mphamvu yanu
Ambuye ndinudi.

Mundionetse, Yesu,
Mapazi anuwo,
Ndidzapondera awa
Munjira monsemo;
Ndithangateni ine
Ndisalefuke ’yi;
Mundilandire m’Mwamba
Ndikamwaliradi.

Exit mobile version