Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 374 NDI lokoma m’Mwambamo,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 374 NDI lokoma m’Mwambamo,

 

NDI lokoma m’Mwambamo,
Mbuye, Bwalo lanulo;
Ndi mwabwino muli ’Nu
Dziko losachimwali;
Mtima wana wonsewu
Umakhumba m’Mwambamo
Nkhope ya Mbuyathuyu,
Mlungu wa chisomoyo.

Zimbalame zonsezi
Zimayamikira ’Nu;
Anthu amakondwanso
Okhumbira m’Mwambamo;
Njiŵa yosapumayo
Inafika m’chombocho;
Okhulupirira ’Nu
Amapuma kwanuno.

Anthu opembedzawo
Amakondwa m’mtimamo;
Munapatsa madzitu,
Munagwetsa manawo;
Mumakoma mtimatu
Tidzayamikiratu,
Pachimpando chanucho
Mkhale Mfumu yathudi.

Exit mobile version