Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 372 DZUŴA la Mulungu

Chichewa Christian Hymns

Hymn 372 DZUŴA la Mulungu

 

DZUŴA la Mulungu
Ladzatu labwino;
Ndi chimwemwe ife
Tiliona lero.
Lithaŵitsa nkhaŵa,
Lichotsanso mantha
Ndimo m’mtima mwathu
Likhalitsa bata.

Tikondwera kuti
Tipumula lero;
Tazileka ntchito
Kuti tipemphere.
Koma ntchito zathu
Za palero lino
Nzakumvera Yesu,
Kumlandira bwino.

Exit mobile version